:Qadianis Hopes Dashed
  Non - Arabic Articles Nayanga/Chichewa

: Qadianis Hopes Dashed
: webmaster

OLEMBA NDI DR. SYED RASHID ALI

           

ASSALAMU ALAYKUM

 

Guulu la Qadinai ndilo sachuka kwa Asilamu ambili: Chi*****wa ndi anthu otsatila mneneri onyenga, Mirza Ghulam, Iyeyu anali wa n’chito wa British Taj kuti aononge chipembezo cha chi Islam kudela la India nthawi ya 19th ndi 20th centuries. Iwowa amati  ndi Aslam koma msogoleri wao kambirimbiri amati aliense otsatira Muhammad (S.A.W) ai ndi Kafir. Tikaonetsetsa guulu la Qadiani ndi lodziwika ndithu kuti iwowo Sali Asilamu, dziko lose lapansi pamodzi ndi alaliki achisilamu ndiponso ndi dziko la Pakistan .

I wowo adaona kuti mpata mwina  uthakupezeka nthawi ya Gen. Musharraf kenaka kusintha kwa Constitution la dziko la Pakistan PCO (provincial Constitution order) yomwe inkafuna kusintha za chipembezo cha chiIslam mu Pakistan, koma guulu la Qadiani ankafuna kuti apeze mpata wakuti naonso aitanidwe kuti ndi Aslam.

 

ALHAMDULILLAH, SIZINATHEKE AI

 

Ifeyo tikali naobe maguulu omwe onyenga ozicha Aslam.Mfano guulu la Qadiani momwe lingo lao pankhani ya mneneri omaliza Muhammad (S.A.W) amati chiani.

Onani tsamba la maulana Maududi =

 http://www.us.edu/dept/MSA/fundamentals/prophet/finalprophet.html.

 

ONANI TSAMBA LA 2

-                      Boma la Pakistan likuti guulu la Qadiani si guulu lachi Islam

-                      Kuononga liu la Islam

 

 1.                  = Chitsimikizo cha 25 February 2000 Friday 18 zulqaad 1420

         http://www.dawn.com/2000/text/nat7.htm

  

BOMA LA PAKISTAN LIKUTI GUULU LA QADIANI SAALI ASLAM

 

Islamabad, 24 February 2000, anthu ose aguulu la Qadiani kapena aguulu la Lahori (omwe odziwika kuti ndi Ahmadi) ai pakadalipano akadalisaslam, izi zamemetsedwa ndi nduna ya zoona malamulo adziko (ministry of Law) tsiku la chinai Thursday.

 Ndunayu anati,  kulingana ndi lamulo la chislam mdziko la Pakistan (clause 3 Article 260 la Constituion, Sali limodzi mulamulo la 14 october 1999 mu Constitution Order No. 1 chaka cha 1999.

 Angakhale zitelo, lamulo la (clause 3 Article 260) la constitution ailikadali lolimba ndithu guulu la Qadiani Sali Aslam ai.

 Nduna yo lankhulira Boma ikali ndithu kuima nganganga kuti guulu la Qadiani sasilamu ai uchokera tsiku la 14th October, 1999. Constitution ikadali chimodzi modzi uteteza mpingo wa chiIslam mokanila za guulu Qadiani (clause 3 Article 260.

 Nduna ya Boma inati, Article 2 ya Constituion order No. ya 1999, ikhale momwemo monga lamulo la boma la Pakistan kuti ndilo lamulo la dziko upyolela mu Constition.

 Dongosolo la malamulo (clause 3 Article 260) la Constution ai likhale lolimba ndithu kotelo kuti aguulu la Qadiani ndi guulu la aLahori (omwe odziwika kuti Ahmadi)sa silam ai mpaka na kalekale ndieno onsewa ndi aslam liti ai. APP

 

2) CHITSIMIKIZO CHA :- MSA UNIVERISTY OF SOUTHERN

CALIFORNIA

 

Quran ndi Sunnah, awa ndiye mabuuku awiri omwe ifeyo tidalira mchipembezo chathu ndi kuitandiwa Asilam okwana enieni. Kodi ndi ziti zoona?

Choyamba ndikuti motsimikiza kuti palibe ompembeza  pokhapo Allah ekha. Ichi ndiye choyamba kwa mslamu aliyense, cha chiwili ndikuti Muhammad ndi mtumiki wa Allah. Onani ziliponso zambiri zotsatira kwa muslam, zonsezi zina zimapanga munthu kukhala okhulupilira mwina osakhulupilira.

Tiyeni tione omwe osokoneza liula Islam ndi Muslim, mwina modziwa kapena mosadziwa. Padakali pano tiyeni tione zipembezo zina zonyenga padziko lino omwe amasewezesa liu la Islam, maguulu awa ndi odziwika upyolera muma buuku awiri Quran adi Sunna.

 Ena mwa awo ma guulu ndi awa:

·  Nation of Islam

·  The nation of Gods and earth (5% nation of Islam)

· The Ahmadiyya /Qadiani movement

·                    The International community of submitters

 

NATION OF ISLAM

 

Guulu la nation of Islam likhulupilira (zonse zomwe iwowo adatunga kapena zolemba)

 ….Mulungu (Allah) mmodzi ndipo iyeyo Allah (God) ada onekera mwa umunthu kwa W. Fard Muhammad, mwezi wa July 1930 omwe adadza Messiah muchi Kristu, mongaso Mahdi mu chiIslam.

 Koma M Quran chapter 4 verse 36 “pembezani Allah, musaphatikize kena kache ndi ye..” Kulingana ndi hadith uchokera kwa Masruq, sahihi Bukhari “Aisha ati, ali yense mwainu onena kuti Muhammad anaonana ndi Mulungu, iyeyo ndi waboza, chi*****wa Allah akuti 6:103 “ALIBE CHITHUNZI SIUNGAMUONE.”

 Guulu la Nation of Islam likhulupiliranso kuti “Uuka kwa kufa osati monga  munthu koma monga wa misala openga. Makamaka anthu akuda (Negroes) azaukitsidwa monga openga amisala, oukitsidwa oyamba. Koma Quran 20:55 ikuti “kudothi tinalenga munthu, kudothiko uzabwelera ndiponso kudothi tikuukisanso.” Onesesa Quran 64:7

 Ndiponso  amati, anthu osakhulupilira sazaukitsidwa tsiku lomaliza (Qiyyama). Koma Quran ikuti “Nena mzina la Mulungu, aliyense azaukitsidwa: kenaka azalamulidwa mchoonadi pazomwe unachita, izozo ndi zapafupi kwa iye Allah.”

Kupyolela ndi zinazache aguulu la nation of Islam, amakhulupilira zonyenga kusi yanisa ndi zomwe zili mu Quran ndi Sunna monga izi,

 Akuti: (Monga ifeyo Aslam akuuda) tikhulupilire kuti “Bibele ndithu ndi yoona, koma mkono wa nthu udaononga malemba kotelokuti ndi kwaife kubwezera zomwe adachotsamo.”

 

Vuto linalache ndi ili: Tikudziwa kuti mtumiki Muhammad wa Asilamu sana lole kapena kuletsa ukhulupilira Bibele kapena kunyalanyatsa baibele – kenaka palibe umboni wakuti tiyeni tibwezere zomwe mkono wa anthu udachosamo ai.

 “Koma ifeyo omwe tinazicha Asilam okhulupirira, tisalowerere kapena kuchita nkhondo yokhetsagazi. Sitiza vomera kuti ifeyo a nation of Islam kupanga nkhondo, chi*****wa palibe phindu lili lonse pokhapo America atalola kuti chitani tero  momwemo mwina tipeza phindu.

 Koma vuto siili, Quran ndi Sunna mabuuku awiri akunena pangwengwengwe kuti Jihad-nkhondo ya chi Islam ilipo ngati nthawi yafika.

 

THE NATION OF GOD’S AND EARTH (5% NATION OF ISLAM)

 

Guulu la nation of Gods and earth (5% nation of Islam) ndilo lochoka mguulu la nation of Islam. Naonso chimodzi modzi nalonso lilipatali ndi chiphunziso cha chi Islam. Vutolao ndi  ili:

 

· Munthu oyamba padziko adali monga mwenye munthu wa kuuda, namalenga, mwini , nthanzi ladziko, bamboo wa

      chitukuko Mulungu wa dziko.

· ..Munthu wa kuuda ndiye Mulungu dzina lache leni leni ndi Allah. Mwini dzanja, mwini mwendo  ndi mwini mwendo, mwini dzanja , mwini mutu.

 

Izizo ndizo chisonyezo cho siyana ndi fundo za Islam, choonadi kuti Allah Mulungu ndiye Mlengi (omwe ankaumba muthu ndi zinazache) nyamalenga.  Quran 25:54 Mulungu Allah akuti, iyeyo Allah adalenga munthu, kotelo kuti munthu sangaitanidwe Allah (mulungu).

 Izi ndiye mmodzi mwamifano yambili yomwe yosokoneza chipembezo cha Islam, koma dziwa kuti angakhale zitelo guulu la nationa of Gods and earths, sanga kwanise kusintha chi Islam. Angakhale masamu kapena chilembedwe, mong Yacob munthu openga ndikuzicha mneneri W.D. Fard, omwe amati munthu wakuuda ndiye wapamwamba.

 Koma Mneneri wa choonad Muhammad (s.A.W) wa Slam , akukanila ndithu zosankhana mitundu pathwawi yache yosazika (Haj):-

 

“Inu anthu! Dziwani kuti Mlengi ndi mmodzi ndiponso Bambo wanu ndi mmodzi. Nonse inu kholo lanu Adam ndipo Adam adachoka ku dothi. Palibe mwainu opambana akhale mu Arab kapena munthu wamba ndiponso munthu wamba ndi munthu wamba apambane mu Arab, kapena anthu oyera apambane anthu akuda kapena munthu wakuda upambana ndi munthu oyera pokha pokha iyeyo okhulupilira.Ndithu ndithu oyera pakati painu niuja wa nzeru.”

 Mbale! Penyetsetsa uyu mwana  The nation of Islam  monga bamboo wache akulephela ndondomeko yachibadidwe, monga malemu  Malik Al-Shabaz

(Malcom X).

 

GUULU LA AHMADIYYA/QADIANI

 

 Guulu la Ahmadiyya lomwe lidayamba ku Pakistan/India mothandizidwa ndi Boma la Britain , ndilo onekela poyera chikhulupiliro chao ndi chopotoza Islam.nsanamina yao ndi yakuti, amakana kuti mtumiki Muhammad (S.A.W) siomaliza ai. Koma tikawerenga  buuku lopatulika la Quran nidi Hadith, tipeza ophunzila pamodzi ndi ophunzila ache anatsimikiza kuti Muhammad (S.A.W) ndiomaliza.

 QURAN IKUTI 33:40

“Inu anthu! Muhammad alibe mwana wamwamuna pakati painu, koma ndithu, iyeyo

ndi mneneri wa Allah ndiponso omaliza mumndandanda wa aneneri . ndipo Allah adziwa zonse.”

 

HADITH: Mneneri wachoonadi wachi Islam Muhammad (S.A.W) akuti

 “Mtundu wa ana a Israel uma sogoleledwa ndi aneneri . Atamwalira mneneri, wina analowa. Koma kulibe mneneri azabwera ineyo ndita mwalira; pokhapokhapo ma Khaliphat (monga olalikira chabe) ndi omwe azapitilira ulaliki wanga.”

(SAHIH BUKHARI)

 Otsatira a guulu la Ahmadyya ndi msogoleri Mirza Ghulam Ahmad waku Qadiani omwe adazicha mneneri ndikumasintha Hadith ndi maayat ya Quran kuti apeze umboni wa uneneri. Mtumiki Muhammad (S.A.W) wachi Islam, anati chenjeza mwaizi kuti:

“Nthawi si izakwana ….pafupifupi ndi 30 “Dajjals” (Onama) azaonekera, omwe azabwela ndiku zicha aneneri otumidwa ndi Allah” (Sahih Bukhari, Sahih Muslim).

 Pambuyopo mwalira mtumiki Muhammad, uyu mwamuna dzina lache Musailama naenso adazicha mneneri, koma adaputidwa nkhondo pamodzi ndi omutsatira ache. Koma angakhale iyeyu ankafuna uneneri adavomera kuti Muhammad (S.A.W) ndi mtumuki ndiomtsatira omwe iyeyo chimodzi modzi anavomera. Chi*****wa chosiyana maganizo ndiye zomwe zinazetsa kuti mtundu wa Banu Hunaifa ndiye omwe udakakamiza kuti uyu Musailima akhale mneneri koma ndio nyenga. Pomwepo nkhondo inauka. Izi zonse ndi zi*****wa zokwana kuti guulu la Ahmadiyya si aslam ai.

 

 

 

Umboni wina onani: http://www.uso.edu/dept/MSA/fund-

amentals/prophet/finalprophet.html

 

Chisanzo china chache kukanila guulu la Ahmadiyya ndi kukana mau a Quran ndi hadith, kuti Yesu anamwalira, ndipo Mirza Ghulam Ahmed anaukisidwa mzimu wa Yesu (incarnation). Koma kulingana ndi Encyclopedia 1985 Britanica, uyu Mirza Ghulam Ahmad anati sindiwe yesu chabe koma mtumi Muhammad, Mahdi kenaka Mulungu wa Batiya ndizina Krishna.

 Koma izi zonse zasiyana patali ndi chipembezo cha Islam chi*****wa chislam sichikhulupulira kuti munthu angakhale Mulungu kapena mwachisoni kukhala Mulungu wa Batiya guulu la chimwenye.

Chi*****wa chaichi guulu la Ahmadiyya ndilotuluka mchipembezo cha Islam mosakaika ai. Kenaka akuti Jihad kulibe muguulu la Ahmadiyya. Chi*****wa ankafuna kuti asaputidwe ndi guulu la aslam enieni koma kuti achinjilizidwe ndi Boma la Britain.

 Werenga upenga kwa guulu la Ahmadiyya Buuku la:-

“Anati Ahmadiyya Movement in Islam Homepage”.

 

THE INTERNATIONAL COMMUNITY OF SUBMITTERS

 

Guulu la Submitters, ndiotsatira Marehem Rashad Khalifa omwe anati naenso ndi mneneri wa Allah. Chi*****wa chaichi guulu ili nalonso silikwana kuitanidwa Aslam.

Quran ikuti : 33:40.

 “Inu anthu! Muhammad alibe mwana wamwamuna pakati painu, koma ndithu, iyeyu ndi mneneri wa Allah ndiponso omaliza mumndandanda wa aneneri. Ndipo Allah adziwa zonse.”

 

 

MNENERI WA ASLAM MUHAMMAD ATI:

 

“Mtundu wa ana a Israel umasogoleledwa ndi aneneri. Atamwalira mneneri, wina analowa. Koma kulibe mneneri azabwera ineyo nditamwalira; pokhapokhapo makhalipha (monga olalikila chabe) ndi omwe azapitiliza ulaliki wanga.” (Sahih Bukhari).

 Vuto la guulu la Rashad Khalifa, ndilakuti, Quran imaenda ndi chiwerengero cha 19. Kenaka anachotsamo ma ayat ena mu Quran monga liu la Allah (God) Mulungu chi*****wa silili mchiwerengero cha 19 monga 19 x6217, yena ma Ayat anachotsamo Mquran onani (Quran 9:129.)

 

QURAN 2:85

 “Kodi Mukhulupirira mbali imodzi ya Quran ndiponso osakhulupilira mbali ina ya Quran? Ndipo malipilo awo omwe opanga izozo za umbuli umoyo wao padziko ndiponso patsiku lomaliza (Qiyama), azaponyedwa mmoto wa Jahena.”

 

Omwe uyu Khalifa ati ineyo ndikudziwa tsikulomaliza (Qiyyama).

Koma Quran ikuti 7:187

“Akufunsa iwe kodi ndiliti tsikulomaliza (Qiyamah) nanga ndi thawi itiizabwera? Nena: Odziwa za nyengo ndi iyeyo Mulungu ekha: Kulibe wina pokhapo iyeyo Mulungu azadzetsa nyengo (Qiyama): Kupindamula kwa dziko ndi mitambo ndi iye Mulungu: izi zonse sizibwera panthawi ino yaiwe koma mwadzidzidzi.Nanga bwanji akufunsa monga iweyo ukudziwa chinsinsi cha chilengedwe.nena: Ekha odziwa za nyengo (Qiyama) ndi iye yekha Allah, koma nonsenu anthu simungadziwe nyengo (Qiyama).”

 

Omwewa aguulu la Submiters akukanila Sunnah kapena Hadith za mtumiki Muhammad (S.A.W) zonse. Guulu la Submitters likuti Hadith ilibe nchito kapena phindu muchi Islam.

 

Chi*****wa chaichi anaononga monga:-

1.         Salati  -Mapemphelo asinthidwa

2.         Zakat  - Mitulo asinthidwa

3.         Swaum – Kusiyakudya kwasinthidwa

4.         Haj – Haj yasinthidwa

 

Guulu ili latenga zinthu 4 kutay akoma livomera nchanamina yo yamba ya Shahadat.

 Kodi guulu ili lingakhale mmodzi mwa slam ? Ai sangakhale Asilam.

 Chenjezo kwaizi, Mtumiki Muhamma (S.A.W.), kuchokera kwa Sahaba Aburafi:

 “Mtumiki Muhammad (S.A.W) akuti: “Asapezeke mmodzi mwa inu atanva zaine zomwe ndalamula kapena zomwe ndalesa kumango ziyesa monga zilibe phindu ai. Gwilitsani nchito Sunnah/Hadith zaine ndi zomwe ndaletsa  lekani ndikusiya.” Vol. 40: 4588 Abu Dawood.

 Funafuna umboni okwana pita:-

 http:www.angelifize.com/journal/aiis

 Kapena

 

 http://www.msa-natl.org/resources/Relief_Orgs.html

 

:   admin       (   )
: 0 /5 ( 0 )

: 26-11-2009

: 2112