عرض المقال :How Mirza Insulted the Holy Prophet SAAW
  الصفحة الرئيسية » مـقـالات الموقـــع » كشف البلية بفضح الأحمدية » Non - Arabic Articles » Nayanga/Chichewa

اسم المقال : How Mirza Insulted the Holy Prophet SAAW
كاتب المقال: webmaster

Bismillah Al-Rehman Al-Raheem

Anti Ahmadiyya Movement in Islam  

MMENE YEMWE ANAYAMBA GURU LA AHMADIYYA ANANYOZERA MTUMIKI MUHAMMAD (SAW)

OLEMBE    DR. SYED RASHID ALI.

 

Zonse zotamandidwa ndi za Allah, umodzi yekha ndipo ndiyemweyo. Chikondi chake ndi madalitso yangagwele mwamuya-ya-ya pa woyela Mtumiki Muhammad pambuyo pache palibe wina Mtumiki.

Anthu a kudziko ya Ulaya (Britain) anatenga mwaupandu ula-mililo wa a muslim wa India sub-contient ndipo lolemekezedwa linatumidwa kudziko la  India ku chokela ku nyumba ya malamulo la ku Ulaya kuti apeze njira yomwe angaletse chikhulupililo cha Jihadi.

 

Pambuyo pa zaka ziwiri zomafufuza, bungweri linapereka zofufuza zao  zomwe mutu wace unati “ Kufunika kuganizila kuti a musilamu abvomere mutsogoreri wao wa ci Islam pa  maso  pao. Lero maganiza  a zopeza munthu emwe a ngazipange ngati mtumiki wansembe. Mirza Ghulam Ahmad anasankhidwa kuti a kwaniritse nchito chi*****wa chakuti anali wa mbado wa anthu a ku Ulaya, ndiponso makharidwe ake ndi chikhulupiriro chace cha za  Mulungu.

 

Anapeza mwa iye munthu wocita zabwino. Patapita zaka, anabvomela mkalata yomwe analemba kwa olamurira wamkulu wa Punjab kuti anangozipanga ku khala ngati Mtumiki wansembe mau  awa apezeka mbukhu lache; kitab-ul-Bariyah. Roohani Khazain vol. 13 p.350 kwa aliyense kuti aone. Mirza Ghulam anakhula kapolo wa Islam, osinthitsa umoyo ndipo anakwela ndime zambiri ndi zomwe zinali kuchedwa Mtumiki. Zikhalidwe zake zinapangitsa kuti apite pamwamba pa mipingo yambiri. Kuyambira pa ukupolo wa Islam, wositha chikhulupililo cha Islam-M’mahadith-Mujaddid- Oringana ndi Eisa ibne Maryam (mueneri woronjezedwa)- Imam Mahdi-Mtumiki wotumidwa- Adam-Sari- Noah- Abraham- Isaac- Ishmael- Joseph- David- Solomon- Jonas- Lord Krishna- Jai Singh Bahadwi, palibe pomwe ankaimirira pothela pache, zikhulupiriro zace za bodza zinamukakamiza kunena kuti anali woyela Mtumiki Muhammad      ndoponso kubwera kwachiwiri. Ndipo analemba : “ Uyo amene asiyamika ine ndi Mustafa sanandione ndiponso  sanandizindikile.” (Roohani Khazain vol. P.259). Lero emwe anayamba ngati kapolo anakhala mfumu mwa iye yekha.

 

Mirza Ghulam Ahmad anakhazikisha guru la Ahmadiyya zaka zikwi-zikwi zapita kumbuyo uku poyendeletsedwa ndi a British kufikira lero lino. Angakhale lero anthu amene apezeka m’gururi aphatikiza aja omwe ali ndi mantha akubwelanso mu  chiIslam. Onse azindikila kuti ngati m’Muslim wachoka ndi kutsata Ahmadiyyah azachepetsa unyiji wa a Muslim. A Muslim amaphunzilo osiyana-siyana ndi a maganizo oasiyana- siyana m’maiko onse ndi ogwirizana muchikhulupiriro cao cha kuti Mirza Ghulam Ahmad anali ochimwa osakhulupirira ndipo sanali m’njira   yachiIslam, ndiponso aliyense omtsatira, angakhali kuti ndi Qadiani, Ahmadi wa ku Lahori, nayeso ndi wochoka mnjira ya chi Islam. Mu nkhani  ya kutha kwa caka ca 1974, ophunzira mwakuya pa za Mulungu analengeza kuti Mirza Ghulam Ahmad ndi onse omutsatira  alibe chikhuhipiriro cha Islam.

Angakhale lero, kuonetsa monga ali a Sunni Muslim ndipo kaswili wa Islam, guru la Ahmadiyyah ipitiriza kunama anthu osaphunzila ndi osanka omwe ali, a Muslim m’balu zosiyana- siyana za dziko. Zolemba zao ziimiliza mbali imodzi mwadala kuyopa zo khulupilira za omwe anayamba gululi.

 

Mwa tsopano apa, pepala linalembedwa ndi ku turutsidwa ndi guru la Ahmadiyyah/Qadianiyah mu mbari zambiri za m’maiko “Ahmad muchitamando  cha zikhalidwe za Indo-Pakistan, maina monga Ghulam Ahmad, Ghulam Rasool , Ghulam Ali Kapena Abdul Rahman ndi ena ndi maina opangidwa ndiponso yatanthauza Ghulam (Kapolo) wa Ahmad, Kapolo wa Rasool, Kapolo wa Ali kapena wanchito wa Rehman (wachifundo). Ndichodabwitsa ndiponso umene Ghulam Kapena Kapolo wa Ahmed alamurira mfumu yake ?

 

Mpepalari mupezeka nkhani zomwe zinalembedwa ndi yemwe anayamba gulu la Ahmadiyya, Mirza Ghulam Ahmad Qadiani, kuyesa kuonetsa kuti anali ledzela ndi chikundi cha woyela Mtumiki Muhammad (S.A.W), odzala ndi zithokoza za Allah, Qur’an loyela la Islam. Zomwe analemba Ghulam simuonetsa munthu wabwino. Koma yamwe Ahmad anali ndi madela awiri osiyana mu umoyo wace.

Dela loyamba linacokela ku umwana wace kufika koyambila kwa ukulu wa umoyo wake. Popeza kuti anabadwa mu banja la Muslim, pa nthawi anali wachikhulupiliro cha Sunni Muslim. Inali pa nthawi imene pomwe ananenelera mobwezara za chikulupiliro cha Sunni Muslim. Inali pa nthawi imeneyi pomwe ananenelera mobwezapo za chikhulipiliro cha Muslim Ahle-Sunnah wal Jammat, ndi chikondi ca woyela Mtumiki wa Islam ndi kufuna kwace kugwila nchito ya Islam. Angakhale kuti analandila maphunziko ache atsopano ku  sukulu    (madrassah) la maphunziko a Mulungu  kapena kuti anapeza ulangizi wa uzimu kulingana ndi mwanabo koma anali kuzithandiza yekha kupanga ziganizo ndi ndakatulo. Ngati kunali kucoka mnjira yokhazikitsidwa ya ahle Sunnah- Jamaat, ici sichinonekele.

 

Pambuyo pace, maganizo ndi zikhulupililo zace zinaonetsa kusintha ndipo anaonetsa kucotsa nzeru kuzomwe anali kunena ndi nthawi, anayambaso kucita zinthu zosayenera ndipo anaonetsa kucotsa nzeru kuzomwe anali kunena ndi kulemba sosaenela a Muslim. Koma kupita kwa nthawi, anayambaso kucita zinthu zosayenela. Ndipo iyi mbali yoipa ya Mirza Ghulam Ahmad inabisidwa ku anthu ndipo sinalembedwe m’mabukhu ya Guru la Ahmadiyya.

 

Mbali ina yomwe ifunika ku  kumbukira ndi zolemba za Mirza Ghulam Ahmad momwe anabvomela kuti anali kudwala matenda osiyana siyana ya mubongo yomwe anali ku  sokoneza maganizo ace . Akunena matenda monga a Machola, Minejaitisi, kuyiwala zinthu mwamsanga , khunyu, chizwezwe, kutaya madzi kawiri-kawiri. Anenanso matenda ena monga unyomwa ndi kusowa mphamvu ya kumvana. Akunena zamankhwala ambiri omwe ankazipangila ndipo ena omwe anali kutenga ku anthu. Akunenanso kumwa zinthu monga mu wine kukhala ngati mankhwara. Anali kulota angelo omwe anali kumuuza mtengo kapena mankhwala ambiri ya kuti amunthandize pakuonjeza mphamu za kumva wace. Ndipo tsiku lina Mulungu anamuuza kuturo kuti akonze mankhwala ya kumwa ndipo chimodzi chomwe chi nali kufunika kusakaniza mu mankhwala amenewa cinali OPIUM.

Kodi analidi odzala ndi chikundi cha Mtumiki oyela ? Kodi anali Mtumiki ? Kapena zinali nchito zace bongo wodwala chi*****wa ca kumwa OPIUM ndi mowa?

M’matsamba yokonkhapo, ndizaonetsa zolembedwa zopezeka m’mabukhu yolembedwa ndi Mirza Ghulam Ahmad kuti owelenga aganizile okha m’mene munthuyu anali. Chizakhala kuti imwe kupeza colinga ca emwe anapeza guru la Ahmadiyyah.

 

MIRZA GHULAM AHMAD NDI MULUNGU WACE

 

Mu zolembedwa zao a guru la Ahmadiyya azionetsa za cikondi ca mtsogeleri wao ndi chithokhozo cha Allah. Kulondora zilembedwe za m’mabukhu mwace zionetsa kuti Mirza Ghulam Ahmad WAHI ndizo khumba zinamulengetsa iye kutenga njira ina.

“ Ndinaona m’maso mwanga kuti ine ndine Mulungu ndikukhulugilira kuti umulungu unalowa mu thupi langa ndipo ndinali kunena kuti tifuna m’mwamba ndi pansi. Ndipo ndinalenga m’mwamba ndi pansi. (Roohani Khazain vol. 13 p.103).

Tsiku lina Hazrat Maseeh Mowood anaulula momwe anali kumvelera. Anaulula izi ci*****wa anali kuzimwera wamphamvu zomwe zalengezedwa ndi Mulungu.

( Trust N° 34, Islam Quarbani p.12 Qazi la Muhammad Qadiani, emwe anali mzace wa Mirza Ghulam).

 

(Subhan Allah! Kunama Allah pa za uwelewele ! Tipemphe Allah aticinjilize pa maganizo otayisa otele).

 

Mulungu Auza Mirza mu wahi wace

“ (Mirza !) Kumwamba ndi pansi kuli ndi iwe monga ku liri ndi ine. Ucokela kwa ine mchigwilizano ndi  kumva ine ndekha. Ucokela kwa ine monga ufumu wanga. Ucoka mwa ine monga mwana  wanga…ndimalakwa ndipo ndimacita zomwe nalengeza…Ndimaima kudwa. Tikupatsa ulemelero wa HAQ monga kuti Mulungu watsika kucoka kumwamba. Tikupatsa ulema wa mwana.”

(Haqiqat-ul-Wahy, Roohani Khazain vol. 22 p.79-99).

 

MIRZA GHULAM NDI MTUMIKI WOYELA MUHAMMAD

 

Mabukhu olembedwa ndi guru la Ahmadiyya ndilodzala ndi zolembedwa za Mirza zomwe zionetsa chikondi cha Mtumiki woyela Muhammad (Sal-Allaho alaihi wa Sallam). Kulondola zolembedwazi m’mabukuwa zionetsa nkhani yosiyana-siyana

Ghulam poyamba anali wa nchito wa AHMAD (MUHAMMAD) pambayo pace analedzela ndi chikondi cake. Kuledzela kumeneku kunaongonga umoyo wace ndipo anakhala Muhammad (SAW). Kodi amene amtsatila (Qadianis/ Ahmadis/ Lahoris/ Mirzais) adziwa  zolembedwazi ? Ngati ali oziziwa, kodi mnjira anazibisa kuti zitsadziwike?

 

Mirza Anena kuti ndi wa nchito (kapole) ndiponso ndi wa chikondi cha Mtumikiti woyela Muhammad SAW.

 

Zolembezedwa mu  kapepala komwe mutu wake ukuti, “Ahmadi athokoza Muhammad,” Mirza akunena kuti ndi wodzela ndi chikondi cha Muhammad (SAW).” Uyu odzicetsa yekha sali Mtumiki kapena otumidwa kupena kapolo olondola.”

(Man a Mirza Ghulam Ahmad, Akhbar Alhakum Qadian N° 23 vol. 5)

 

pambuyo pa Mulungu ndi oledzela ndi chikondi cha Muhammad. Ngati uyu simusilamu, Mulungu wanga ndine munthu usayenela.

(Zokambidwa za Mirza mpepala : “Ahmad nichithokozo wa Muhammad, p.1).

 

atanetsa omutsatila ake za chikondi wache cha Mtumiki woyela Muhammad (SAW), anapitiliza kuonetsa kuti, chikondi cake casandutsa thupi lake kukhala limodzi ndi thupi la Muhammad. Ndipo Mirza anati :

“ Allah anandipatsa udindo wa Mtumiki oyela ndipo anandipangitsa mtima kwa Mtumiki wacifundo wa kuti ine ndinakhala monga njira. Lero amene a tsata jamaat yanga akhala m’modzi wa sahaba ya juma yanga yomwe inali kuposa Mtumiki onse. Sichili chinthu chobisika kwa aja amene akwanitsa kuganiza kuti uku ndiko kutantha uza kwa mau asiyanitsa ine ndi Mustapha (Mtumiki woyela pbuh) akalibe kundiona ndipo sandidzindikila.

(Khutbah-e-Ilhamjah, Rohani Khazain, vol 16- pp.258-259)

 

kunali cabe kulindila nthawi ndipo anayamba kunena kuti anabadwa kutenga mulo a Mtumiki woyela( SAW). Lero GHULAM ANAKHALA  MFUMU.

Mirza Ghulam Anena kuti ndi Muhammad (SAW)

Mirza Ghulam akuti :

“Mtumiki woyela ali kubwela kawiri kapena tingati kuti kubwela koyumba kunatsimikidzidwa ndi kubwela kwa Messiah olengezedwa ndiponso Mahdi olengedzedwanso.”

(Roohan Khazain vol 17. p.249)

 

Mirza Ghulam anati :

“ Ndakhala ndikunena nthawi zambiri kuti kulingana ndi ndime (ya mu Qur’an oyela)”. Wa akhareena minhum lamma yalhayoo behim’as Buwoz, nditi Mtumikii m’modzi-modzi, Khatamul Ambiyyah ndipo zaka makumi awiri apitapo Mulungu anandipatsa dzina lakuti Mohammed ndi Ahmad mu Baraheen-e-Ahmadiyya ndi kupanga ine kukhala iye.

(Aik ghalti ka azala, Roohani Khazain vol 18 p.212).

 

Mirza Ghulam anati : “Mtumiki oyela anabadwa kawiri monga Mtumiki. Mkunena kwina tingati kuti chinalengedzedwa kuti Mtumiki woyela(SAW) adzakabadwanso mdziko ndiponso ichi chinatsimidzedwa ndi kubadwanso kwa Messiah olenjedzedwa ndiponso Mahdi.

(Tohfa-e-Golrwia, Roohani Khazain vo 17 p.249).

 

Mirza anati:

“ Pamene ndiri Mtumiki woyela obadwanso kwa chiwiri, ndipo zonse pomwe zinacitidwa ndi Muhammad kuonjezapo za utumiki, zioneka ngilasi kapena cilola changa, telo ndani wina emwe anganena kuti ndi Mtumiki mwa iye yekha ?”

(Ek Ghalti ka Izala, Roohani Khazain vol 18 p.212).

 

Zikhulupililo zotelezi ndi zilembedwe za Mirza Ghulam Ahmad zinapangitsa kuti omutsatira ace kuti anene mopanda manyazi zikhulupiliro zao.

Mirza Basheer Ahmad s/o Mirza Ghulam a kuti: Maseeh Mawood salephera kulota ku Mtumiki woyela (pbuh), koma ndi iye amene abwera ku chiwiri m’dziko monga Buroozi…lero kodi palichikaiko ca kuti Mulungu watuma Mtumiki woyela kachiwiri ku Qadian ?

(Kalimat Alfasl p.104-105. Review of Religions Qadian March 1915).

 

“Tsopano ndi chicodziwika kuti kukana Mtumiki  woyela ndi KUFR ndiponso kukana Messiah olonjedzedwa ndiponso KUFR, chi*****wa Messiah sasiyana ndi Mtumiki woyela. Koma ndiye  ngati iye akana Messiah sali KAFIR terenso amene akuna Mtumiki  woyelanso kafir, Mulungu aletsa.”

(Kalimat alFasl p.146-147. Review of Religions Qadian, March- April 1915).

 

“Kodi kuli cikaiko cotsala cakuti Mulungi watuma Mtumiki (pbuh) kwa chiwiri mu Qadian ku nsimikiza chilonjezo?”

(Kalimat al Fasl by Mirza Basheer Ahmad. Review of Religions p.105, N° 3  Vol 14).

 

Mirza alingana ndi Mtumiki Woyela Muhammad

Inali njira ina yofuna ku zilinganiza ndi Mtumiki  woyera. Mirza anati :

“Aliyense yemwe asiyanika iye ndi MUSTAFA (pbuh) Sanandione ndipo Sandiziwa.”

(Roohani Khazain, vol  16 p.171)

 

Ololedwa kupambilako Qadiani, Al-Fazl analemba kuti :

“ Chikhaliro cha olengezedwa Maseeh (Mirza) nimaso mwa Allah ndi chikhaliro wa Mtumiki woyela (SAW). Mchikumbukilo china,mzosungidwa za Allah kulibe kusiana pakati pa Messiah olengezedwa ndi Mtumiki woyela (SAW). Koma onse agawana mpando olingana ndipo ali ndi dziko limodzi. Angakhale kuti nimakambidwe ali awiri, awa ali m’modzi ndipo olingana.”

(Al-Fazl, Qadiani, vol. N° 37 dated 1e  September 1915, as cited in Qadiani Muzhah page 207, ath edition-Lahore).

 

QADIANI KALIMA.

Mimalembedwa a oyamba zinapangitsa nikhulupiliro izi :

“ Mkubwela kwa Messiah olengezedwa, kusiyana kumodzi kwapezeka ndipo ndikwa kuti akalibe kubwela ka chiwiri kwa Messiah olengezedwa, mcitanthauzilo kwa’Muhammadur RassuLullah’ Atumiki chabe amusiku akumbuyoku anali anaikidwapo, koma mkubwela kwa chiwiri kwa Messiah olonyezedwa Mtumiki umodzi waonjezedwapo pa tanthauzo la Mohammadur Resoolulah’…tero kumva mu Islam ndi kalima yemweyu, kusiyana kwekha komwe kulipo ndi kwa kuti kubwela kwa chiwiri kwa Mtumiki kutanthauzo lache…sifuna kalima watsopano, chi*****wa Messiah wolonyezedwa sali opatuka kucokela kwa Mtumiki woyela monga ali kunena ‘Saara wajuodi wajoodahoo (Manthu wanga anasanduka munthu sanandine ndipo Sandizindikila’ … telo Messiah iye amene abwela ka chiwiri m’dziko lino kuzafalitsa chi Islam, lero sitifuna kalima aliyense wa tsopano  ngati wina anabwela ndiye kuti modzi tinafuna…telo onse muyenela kuganiza.”

(Kalimat Al-Fasl p. 158 na Mirza Basheer Ahmad).

 

Chi*****wa ca kubadwa kwa Messiah tiolenjezedwa (Qadiani Mirza) kusiana kwabwela (mcitantha uzo ca Kalimah). Akalibe kubadwa Messiah olonjezedwa (Qadian Mirza) m’dziko monga Mtumiki, Mau akuti Muhammadur Rassolullah anaphatikiza mtanthauzo lawo, okhao aporofeti omwe analiko iye akalike kubwela; koma pambuyo pobwelanso kwa Messiah olonjezedwa (Qadiani Mirza) Kwa chiwiri m’maiko monga Mtumiki, Mtumiki umodzi waonjezedwa ku tanthauzira la Muhammadur Rassoolullah. Lero mkulinganandi kuukanso kwa Messiah olonjezedwa Kalimah, Mulungu akana, sikuthesedwa kuna kuwala kuposa. Mwa chidule, Kalima ameneyu ali ndi mphawu m’mpingo tsopano polowa  MuchiIslam. Kusiyana kwache kwa  kukhalanso ndi thupi la Messiah olenjezedwa (Mirza Qadiani) aonjezela Muhammadur Rasoolullah.” (Kalimatul Fasl page 158, Mirza Bashim Ahmad  Qadiani).

 

Kuonjezelapo, angakhali kuti tivomera pakuganizira zomwe sizingacitike zakuti zina lolemekezedwa la Mtumiki(pbuh). wolonjezedwa mu kalimah chi*****wa cha kuti ye ndi othela wa atumiki, angakhale lero palibe choipa ndipo sitifunanso Kalima watsopano chi*****wa cha kuti Messiah wolanjezedwa salipayekha kuchopa pa Mtumiki pakuti iye (Mirza) yekha a kuti; “ Ine ndi chimodzi-modzi ndi Muhammadur Rasoolullah.” Ndiponso “Iye amene a patula pakati pa ine ndi Mustafa Sandidziwa ndipo Sandiona.”

Chomwe wamkulu Allah analonjeza, cha kuti  azambwenzanso”Khatam-un-Nabiyeen m’dziko lino ka chiwiri monga Mtumiki  momwe olonjezedwa Mtumiki Messiah (Mirza wa Qadiani) mwa iye Muhammadur Rasoolullah, amene anabwelenso mdziko kaciwiri kumwaza uthenga wa Islam. Lero sitifuna Kalima watsopano.

 

QADIANI DUROOD SHAREEF

“ Lero mkulingana ndi malembedwe a Qur’an, ‘anthu achikhulupiliro’ tumani Salaat yanu kwa iye ndipo mulambile iye ndi ulemu (33:56) ndipo mkulingana ndi ma Hadiths amene muli malamulo atumila Durod kwa Mtumiki woyela pbuh, kutuma Durood kwa Hazrat Maseeh Dawood nkofunikila momwe muliri kofunikila kwa Mtumiki woyela pbuh.”

(Risala Durood Shareef-Mohd Ismael Qadiani p.136).

 

Mkulingana ndi zikhulupiliro za Islam ndi ma Hadith, nkojunikila kuonjezela M’baja lache (Mtumiki woyela pbuh) mu Durood. Chimodzi-modzinso nkofunikila kutuma Durood kwa Maseeh ndipo osakhala okhutila ndi Durood yomwe iya m’fikira iye (Mirza) angakhalenso ngati wina watuma Durood kwa Mtumiki woyela pbuh. Telo Hazrat Maseeh Mowood akuti :

“ Chimodzi pa zimene zikanidwa ndi ayah amene (Mirza) agwilitsila kwa iye ma akuti ‘alaihe assalato wa assalam ndipo kunena telo ndi HARAM. Yankho kwa ici ndilakuti ine ndine Mtumiki wolonjezedwa, ndipo ndiika pambari zikambidwa za Salaat and Salaam, Mtumiki woyela iye anati  amene amupeza, apeleka Salaam lache kwa iye ambiri, Salaam-o-Salaam yothokozera  Messiah olonjezedwa.

Pamene mau otelewa okhuza za  amenewa ndi Mtumiki, sahabah anati, Mulungu ndiye anati,lero chingakhale bwanji haram jama’at yanga kunena mau otelewa kunenela ine.”

(Risala Durood Shareef, Arba’een N° 2 Roohani Khazain vol. 17 p.349).

 

Mirza atengela zilembedwa za Qur’an Loyela.

 

Uyu munthu ozinenela yekha kuti akonda Mtumiki woyela mothelatu anayamba ziululidwa mwa woyela Mtumiki Muhammad (SAW) kumuululika kuti zonse zolembedwa ziululidwa mwa Mirza Ghulam pa ulemelelo wache.

 

Ngati mwatsegula mu Haqeeqatul Wahy mu Volume 22 la Roohani Khazaini muzapeza kuti pa matsamba 77 kufikila tsamba 111. Mirza Ghulam anena za ziululidwe zace maka-maka mchitundu cha Arabic. Omwe adziwa zilembedwe za Qur’an azadzindikila mwa muisanga za kulengela kwa matembedwe a bukhuli. Mkati mwa zolembedwamo, muli ziululidwe zomwe zinalembedwa kuthokoza woyela Mtumiki Muhammad ndi zina zinagwilitsidwa  Hazrat Ibrahim (AS). Ndi dzitsanzo cabe zingono zomwe ziza kambidwa.

 

Allah athokoza Mtumiki woyela Muhammad (pbuh) ndi anzake mu Qur’an loyela m’malembechwe awa :

“Muhammad Rasuulullah wal ladhina m’ahuu, ashiddau’alal kuffur rahman bainahuù.”

Muhammad, mtumiki wa Allah ndi aja omwe ali naye.  (Al-Qur’an 8-29)

 

Mu zaka zikwi-zikwi zapita kumbuyo uku, Ma Muslims sana khale ndi chitanthaulilo china cha verse kapena zilembedwezi koma WAHI wa Mirza amvuza kuti :

“ Muhammad Rasoolullah wal Ladhiina m’ahuu ashiddan’ala kuffaar whaman bainahum mchiutlidwe ici Mulungu andipatsa dzina lakuti Mohammed ndipanso Mtumiki.” (Roohani Khazain vol 18 p.201)

 

Zotsatira ndi nindakaturo za zilemedwe za Qur’an loyela zomwe ense mu Muslim okunda Mtumiki adzadzidzi ndikala mwamsanga kuti athokoza Syedna Muhammad (SAW), zinaulidwanso kaciwili kuthokoza Mirza Ghulam Atelo Mirza :

“ ‘Huwa Iladhi arsala rasuulahu bil huda’ Iye mulungu neliye watuma mtumiki ndikumulangiza zacita.” (al-Qur’an p:33)

 

“Subhana Ilahi asraa bi’abdihii…alemekezedwe Allah amene anatenga kapolo wache usiku pa ulendo wopita ku Masdjid AlHaram kupita ku Masjidal Aqsa…” (al-Qur’an 17:1)

 

“ Qul in kuntum tuhibbunallaha fatabiun” akuti (O Muhammad) Ngati umukonda zoona Allah, undilondele” (al-Qur’an 3:31)

 

“ Inna fatahua laka fata-han mubiina.” (al-Qur’an 48:12)

 

“ ‘Ya Siin walaalin Hakim. Innaka la minal murSaliin… Yassen ! Zoona inu Muhammad muli m’modzi mwa atumiki.” (al-Qur’an 36:1-3)

 

“ ‘Inna aatainaakal Kawsar…’ Tamupatsaini inu mtsinje mu paradiso…” (al-Quran 108:1)

 

“ ‘Wa arsal naakal ila rahmatan lil aalamiina.”

Ndiponso sitinakutume kuti ukhale wachifundo kwa onse ni calo.” (al-Qur’an 21: 107)

 

Atatenga udindo wa woyela Mtumiki (SAW), anayamba kudzipatsa iye tyekha uzidindo wina :

·         Mbanja lace linakhala AHLE BAIT

·         Anzake anakhala a Sahabah

·         Mkazi wace anakhala umm-ul-m’OMINEEN

·         Mosque yomwe inamangidwa ndi atate ace inakhala al-AQSA MOSQUE QADIAN.

 

Kwa zaka zikwi-zikwi (1400 yrs) a Muslim sandziwa bwino za zobisika za dziko loyela la Jerusalem. Ndipo mkulingana ndi Mirza Ghulam Masjid Aqsa, Qadian Mtumiki woyela anapita ku Qadian osati ku Jerusalem pa usiku wa Ascension Mirza akuti :

 

“ Munalembedwe mu Qur’an loyela (17:1) ‘Subhan alladhii asra bi’abdihii lailammin al Masdjid al Haram ila al Masdjid alAqsa…’ Ulemu kwa iye amene anatenga kapolo wace usiku kunicotsa kwa Masdjid Haram kumpereka kwa Masdjid Aqsa…Kutanthauza kuti Mosque inamangidwa ndi atate ake a Mirza ndipo ku kulitsidwa kwace kwapangidwa ndi Mirza.”

 

Qadiyan inakhala yocilizidwa monga ARDh-e-JARAM ndipo kuyendela malowa kunakhala cithoozi cha Hajj:

“ Malo a Qadian  ndi lemekezedwa. Khamu la anthu lalipanga kukhala malo a Haram.” (Mirza Ghulam’s poetry Dur-e-Sameen p.58).

 

Anthu anapita ku superogatory (Nafy) Hajj. Koma kumalowa (Jalsa Salama mu Qadian) ndipo lace ndilopambana NAFIL HAJJ ndipo kusaikila nzelo sikwabwino pakuti njila yake (Ahmadiyya) ndi yabwino ndipo zamtendere zichoka kwa Mulungu. (Alna-e-Kamalat-e-Islam. Roohanni Khazain vo. 5- p.352)

 

Pakuti okhao amene ali olemela ndiamene akwanitsa kupita ku Haji, osauka amewa lephela kupitako.Lero Mulungu waikapa ZIL HAJJ kotelo kuti aja omwe ajuna kutukuta chikhulupililo cha Islam ndi aja osauka a Muslim a ku India naonsO angapezekeko.” (Khutba Mlan Mehmood Ahmad Khalifa Qadian, Pepala la Alfazl vol.20 N°66 lolembedwa pa 9 Dec. 1932).

 

Ndipo Pothela, koma osati chothelelela, omwe anatenga mpando pambuyo pake anakhala “Khulafa-e-Rashideen.”

الصفحات [1] [ 2]

اضيف بواسطة :   admin       رتبته (   الادارة )
التقييم: 0 /5 ( 0 صوت )

تاريخ الاضافة: 26-11-2009

الزوار: 4672


المقالات المتشابهة
المقال السابقة
Writings Speak
المقالات المتشابهة
المقال التالية
AlFatwa No. 8
جديد قسم مـقـالات الموقـــع
القائمة الرئيسية
البحث
البحث في
القائمة البريدية

اشتراك

الغاء الاشتراك