عرض المقال :How Mirza Insulted the Holy Prophet SAAW
  الصفحة الرئيسية » مـقـالات الموقـــع » كشف البلية بفضح الأحمدية » Non - Arabic Articles » Nayanga/Chichewa

اسم المقال : How Mirza Insulted the Holy Prophet SAAW
كاتب المقال: webmaster
"margin: 0in 20.9pt 0pt 35.4pt; text-align: justify" class="MsoNormal"> 

Wahi la Mirza Ghulam

Pa nthawi Mirza anatha matha ndipo anali kukamba momasuka za zikhulupiliro zace. Telo anaulula za WAHI lake.

“ Chomwe chipangitsa zikhulupililo zathu si Hadith ichi koma Qur’an ndi Wahi yomwe ibwela kwaine. Inde, nikuonjezako tilangiza aja ma Hadith omwe ali nikulingana ndi Qur’an ndipo satsutsana na WAHI langa. Ma Hadith ena, ndiataya kutali monga pepala ilibe nchito.”

“ Mu Braheen-e-Ahmadiyya, Mulungu aniitana nidzina la Ibrahimu.” (Arba’een n° 3. Roohan Khazain, vol 17 p. 420).

 

“Zophunzitsa zanga ziphatikiza malamulo ndipo ziletsedwa ndi zifunilo za Shari’at. Pa chi*****wa ici, Mulungu apatsa dzina Wahi yanga ndi zomwe ndi chita lakuti ‘bwato’. Telo unani ndi zikhulupiliro zanga ndi kuti ndine chombo cha Noah ndi chopulumukilamo cha anthu onse. Lekani yemweali ndi matso aone ndipo amene ali ndi matu anvele.” (Arba’een vol. 4 p.6 Roohani Khazain vol. 17 p.435).

 

“ Ndinena molumbila kwa Mulungu kuti ndikhulupilila mu zomwe ndichita monga momwe ndikulupililanso Qur’an ndi mabukhu ena a Mulungu. Monga momwe ndikhulupilila Qur’an mosakaika kuti ndi bukhu la Mulungu, Chimodzi-modzinso ndikhulipilila kuti Wahi ija yomwe itsika mwa ine ndi Mau a Mulungu. (Haqeeqat) Wahi Roohani Khazain vol 22 p.220)

 

“Chikhulupililo changa mu Wahi chilingana ndi chikhulupililo comwe ndili nacho mu Qur’an ndi Torah.” (Haqeeqatul Wahi, Roohani Khazain vol.22 p.401)

 

Mirza ndiopambana pa Mtumiki woyela Muhammad SAW (ma’azAllah):

Mirza Ghulam Ahmad anali akali osakhutila. Anali kufuna kupitililapo. Chomwe anacita cholondolapo chinali chozikutitsa kupambana Mtumiki woyela Muhammad (SAW). Ndipo anati :

“ Koma ceni-ceni ndi ca kuti za uzimu za Mtumiki woyela  pbuh (mwa Mirza Ghulam) Kuthela malemba ya chisanu ndi kamodzi, ndi zamphamvu kwambiri mkulinganiza ndi zaka zakumbuyoku. (Khutba-e-Illhamiah, Roohani Khazain vol.16 p.271)

 

Za nzimu za mporofeti wathu oyela (SAW) zinali zobisiku mu 5th thousand (Makk’i birth) ndipo nthawiyi sinali yapamwamba mkukula kwa zauzimuwace. Koma uku kunali koyambilila kufika pa mwamba-mwamba pa tsanja ya zabwino. Pambuyo pace, za uzimuzi zinafika pa chimake mu 6 th thousand (Kubadwanso kwace mu Qadian) pa nthawi imeneyi. (Mirza in Khutba-e- Ilhamiyah, Roohani Khazain vol. 16 p.266).

 

Anthu omwe anali kumtsata anawauza kuti anapatsidwa zi zindikilo ndi zodabwitsa zokwanila 300 000 pamene Mtumiki woyela anapatsidwa cabe 3000. Mozikuza yekha, analemba kuti : “Kwa Mtumiki woyela, Mulungu anamuonetsa cabe eclipse ya Mwezi. Koma ine anionetsa Ma Eclipse yonseya Mwezi ndiponso ya dzuwa, lero kodi simudzandikhululupililila?” (Aijaz-e-Ahmadi, Roohani Khazain vol.19 p.183)

 

Ananena kuti zambiri zobisika za mu Qur’an kapena zinanthauzo za cinsinsi sizinachulidwe kwa Mtumiki woyela (SAW) koma iye wauzidwa pa izi. Tele Mtumiki woyela sanadziwe tauthauzo la Ibne Maryam, Dajjah, Donkey dajjah, Gog ndi Magog, Daabah) Ardh. (Izala-e-Auham, Roohani Khazain vol 3 p.473).

 

“Uisilamu wa Mtumiki woyela unaoneka ngati  Mwezi wa tsopano (Mthawi ya Mirza) ndipo unali kuyembekezedwa kasanduka monga mwezi odzala.” (Roohani Khazain vol 16 p.184)

 

“ Nchodziwikilatu kuti Fath-e-Mubeen anabwela pa nthawi ya Mtumiki wathu ndipo kupambana kwima kunatsala komwe kuli kwa kukulu ndi kodziwikilato ndipo nthawi yace ndi nthawi ya Messiah wolonjezedwa.” (Roohani Khazain vol.16 p.288).

 

Chinenedwe ici cinanenedwa pamatso pa Mirza ndi anthu omwe anali kunitsata. Kwanenedwa kuti Mirza anati : Jazakallah ndipo atalemba malembedwe a bwino, anapachika zolembedwazi m’nyumba yace.

 

“ Muhammad watsikanso pa ife ndipo ndiochuka kuposa kale. Amene afuna ku muona iye bwino-bwino ayenera kuyangana Ghulam Ahmad mu Qadiyan;.” (Qazi Zahoor Ahmad Akmal Qadiani yolembedwa mu pepala la Paigham-us Sulh- 14th March, 1916).

 

“ Kukula kwa nzeru kwa Messiah wolonjezedwa (Mirza of Qadian) ndi kupambana Mtumiki woyela (pbuh). Iyi ndi mbali cabe ya kukula kwa Messiah wolonjezedwa kuposa Mtumiki woyela.”

 

Mirza apatiliza kumcepetsa Mtumiki oyela Muhammad (SAW).

 

Mtumiki woyela sanadziwe tanthauzo la Surah Azilzal (Roohani Khazain Vol 3, pp;166-167)

Zomwe anaulula Mtumiki woyela zinasanduka zaboza. (Roohan Khazain Vo l3 p.472)

Mtumiki oyela analakwa mkumvetsa kwa zouliludwa (Roohani Khazain Vol 2 p.224).

 

Manda a Mtumiki woyela ndi malo oyopedwa kwambiri ndi a Muslim dziko lonse.

 

“Lero Mulungu anatsankha malowa kuti aikepo Mtumiki  woyela (pbuh) omwe anali oipa ndipo onunkha kwambiri ndiponso  wamdima, malo umwe anali odzala ndi matubvi atidoyo…” (Roohani Khazain Vol 17 p.205).

 

Akuzipanga kuti ndiye Mtumiki othela.

 

Pa nthawiya, Sichinali choodabwitsa kuti anali kunena kuti ndi Mtumiki othela.

“ Mwa nthawi zambiri ndakhala ndiri kunena kuti nikulingana ndi verse, ‘Wa aakhareena minhuru lamma yalhaguo belim-ndi ena omwe akalibe kuzionjezela pa iwo…’ (al-Qur’an 62:3) mu BUROOZI, halili Mtumiki m’modzi-mdozi KHATUM-UL-ANBIYA (othera wa Atumiki). Zaka makumi awiri apita kumbuyoku Mululngu ananicha Muhammad ndi Ahmad mu Braheen-e-Ahmadiyya ndikunena kuti ndine Mtumiki woyela (pbuh) omwe atenga nalo a Mtumiki emwe analipo. Lero Utumiki wanga siutsutsana ndi Utumiki wa Mtumiki woyela (pbuh) wanga Mtumiki  wothela chi*****wa cha kuti nkosatheka kupatula cithunzi, kuchoka ku chinthu chomwe chapanga chithunzico pakuti ndi chinthunzice cha Muhammad, lero ndiri Mtumiki wotsiriza pakuti Utumiki  wa Muhammad unatsala ndi Muhammad.” (Mirza Ghulam in Ghalti ka Izala, Roohani Khazain vol 8 p.212 ).

 

“ Niodala iyo amene andidziwa . Pa njila zonse zopita kwa Mulungu ine ndine njile yothela, ndipo pa zowala zace, ine ndine njila yothela, ndipo pa zowala zace, ine ndine kuwala kokhela. Koma tsoka kwa iye amene satsata ine ci*****wa chakuti popanda ine, zonse zili munidima.” (Kashti-e-Nooh, Roohani Khazain vol 19 p.61 ).

 

“ Ndine ndekha demwe wasankhidwa mu Ummah kutenga dzina la mtumiki.” Palibe wina aliyense amene angapatsidwe dzinari…ndipo dzinari kufuna kuchitidwa…monga momwe zinanenedwa mu Sahihi Hadith kuti kuzakhala cake munthu ekhayo nimodzi ndipo  chinenedwechi chatsimikizidwa.” (Haqiqeetul Wahy; Roohani Khazain Vol 22 p.401).

 

Umtumiki unathela pali mtumiki wathu (pbuh). Lero mpambuyo pace palibe Mtumiki  wina  kuchotsako yemwe wakudziwa ndi kuwala kwace ndipo wapangidwa kutenga inalo ace ndi Mulungu. Dziwani kuti kumathelo kunapatsidwa kwa Muhammad (pbuh) kucoka pa chiyambi  ndiku patsidwa kwa iye (Mirza) amene anaphunzitsidwa ndi uzimu wace ndikumupa chithunzi cace. Lero diodala amene aphunzitsa ndiponso  ndiodalanso amene amphunzira (Mirza) . Lero Mthero anaikidwa mu Malembamu ya chisanu ndi  kamodzi. (Zamima Khutba Ilhamiah, Roohani Khazain vol 16 p.310).

 

Mirza BasheerAhmad s/o Mirza Ghulam analemba kuti:

“ Lero munthu m’modzi yekha anatenga udindo wa Utumiki mu Ummah wa Muhammad… kucotsako cabe Messiah walonjedzedwa (Mirza) kulibe wina analondola Mtumiki  woyela. Motelo, ndi Messiah olonjezedwa cube amene anasankhidwa kuchedwa mporofeti.” (Kalimat Al-Fast, Review of Religions, Qadian p.116 N° 3).

Magazini yololedwayo Qadiani analemba kuti :

“ izi zolembedwa  zionetsa kuti ndi Messiah cabe wolonjezedwa amene angakhale Mtumiki… Pambuyo pa mporofeti oyela (pbuh) Mtumiki nimodzi cabe anali kufumka ndipo kubwela kwa a Mtumiki ambiri kunakazokoneza zifunilo za Mulungu ndi zomwe anali kufuna kucita.” (Tasheed-ul-azhan, Qadian, n° 8, vol 12, pp.11, August 1917).

 

Mirza Adzudzula Islam

CHI  ISLAM   CHOMWE  CHINALIKO   MIRZA   AKALIBE   KUBWELA NDI CHI ISLAM   CHAKUFA

 

Maka-maka mu chaka  cha 1906, mwa maganizodwe a Khwuja  maluddin, Moulvi Muhammad Ali analowa nchigwilizano ndi mkulu wa Akbar-e-Watan (wowona pa zilembedwe) kuti aone kuti zolembedwa zao siziulutsa za cikhulupililo ca ka guru ka Qadiani. Zolembedwa zinali kufunika chabe kuulutsa za cikhulupiliro cha Islam. Olonjezedwa Maseeh anakana zamaganizo awandiponso a Jamaat naonso, Hazrat Sahib anati.”

“ Muzanena za Islam mu dziko mosandiikako ine?.” (Zikr-e-Habib by Mufti Muhammad Sadiq Qadian p.146. First Edition).

 

“ Tikhulupilila kuti mpingo yomwe alibe chiphupirio cha Utumiki (Monga mu Islam) ndi mpingo yakufa. Tunanena ma religion ene monga ma Yahudi, ma christu  ndi ma Hindus kuti ndi m’mpingo yakufa chi*****wa cha kuti alibe Mtumiki .Kodi nchi*****wa ninji tinena kuti Islam ndiyopamnana pa m’mpingo ena onse ?” Iyenela kuti isiyane.” (Malfoozat-e-Mirza, Vol.10 p.127).

 

MIRZA ANENA KUTI ISLAM NDI YACABE-CABE NDIPO NDI YA USATANA

 

“ Kuti mpingo si mpingo ndi Utumiki si Utumiki pakulondola munthu amene salipafupi ndi Mulungu kuti apatsidwe mphamvu zace. Kuti mpingo ndiwa chabe-cabe yomwe uphunzitsa anthu kuti chitukuko cha munthu chiyembedwa cabe pa zomwe zilembedwa mu Qur’an loyela ndi mu Shari’at-e-Muhammadia yomwe inanenedwa ndi Mtumiki woyela (pbuh) ndipo kuti ‘WAHI’ yatsata mu mbuyo m’malo mopita pa tsogoro… lero chimpingo chotere  chiyenekela kuchedwa kuti ndi chansatana osati cha  Mulungu. (Zamima Braheen-e-Ahmadiyya, part  V. Roohani Khazain Vol 21 p.306).

 

“ Ndi chodabwitsa kukhulupilila kuti pambuyo pa Mtumiki woyela (pbuh) Chitseko cha ‘wahi’ chatsekedwa ndipo kulikenso chiyesezelo chanaco mpaka tsiku loika-lamba cabe . Kuli mpingo yomwe sikhuzana ndi wamkulu Allah yomwe ingachedwe mpingo ?… ndinena mwa Mulungu wamkulu, kuti nimasiko ano, kulibe amene ati nkhidwa kopambana ine mu mpingo yotere. Ndinena mpingo wotereyi  ndiusatana  ndipo  kuti   mpingo   ya  jehena  ya  kumoto ndikutseka maso a munthu mpaka kufu kwache.” (Zamina Braheen-e-Ahmadiyya part V).

 

MIRZA NDI QURAN YOYELA.

 

“ Qur’an ndi bukhu la Mulungu ndi mau amukamwa mwanga.” (Adversement dated 15th March 1897, Roohani Khazain vol 22 p.87).

 

pamene Mirza Ghulam Ahmad anaudzidwa kuti zolembedwa zace zinyoza aja amene anali kutsutsana naye, anane kuti Qur’an nayonso ili ndimau ambii vipa ndipo anafotokoza kuti sanali kufikako pa zofunikila za masiku ano. (Roohani Khazain Vol 3 p.115-117 ).

 

ZOSINTHIDWA   MU   QUR’AN   YOYELA

 

Pali njira zambiri zomwe izi zingantidwe:

Kusintha  kwa mau

Kusintha  kwa zitanthauzo

Kusintha  kwa zindime

Kucotsa zikakamizo za Qur’an

 

Mirza Ghulam Ahmad anapezeka ndi milandu yonse inai. Angakhale kuti sanasithe ziri zonse zolembedwa mu Arabic m’bukhu la Qur’an, koma m’malembedwa ace ocotsa mbukuli, asintha mwadala zina zolembedwa mwa Arabic. Zitsanzo za zina za lembedwa mu matsamba otsatila.

Chitsanzo chodziwika kwambiri pa zosinthidwa za matanthauzo a Qur’an loyela ndi ndime la 3 : 144  lomwe linene  pa KUTHA KWA UTUMIKI

Kuchoka pa chiyambi cha Islam, pa nthawi ya Mtumiki  woyela Muhammad kufikira lero lino, onse ma Muslims anaciona chinthu chosasokoneza pa MirzaGhulam Ahmad yemwe mu zaka zoyambilira anali ndi chikhulupiliro chotere. Koma pambuyo pace pomwe maganizo ace anasintha, anapatsa chinenero chotere cha kuti Utumiki wa Muhammad siunathero koma masegulidwe a Mtumiki amtsogolo, Monga kuti ALLAH, yemwe  anatumiza Atumiki 124.000 la amupatsa udindo Mtumiki woyela Muhammad. Atero anena kuti ndiye adzakhala Mtumiki wotsatiripo, kuunika kokhera pakati pa kuunika konse kwa Allah. M’manenedwe ena, zonse zokambidwa zosokoneza mitu zomwe anapatsa m’mabukhu ache mu ndime imeneyi zinali zofuna cabe kupititsa pa tsogolo Utumiki wace. Atsegula chitseko cha KHATME NABUWWAT, alowa ndiponso atsekanso. Kodi sichitsanzo cha chikuri chakuba chimeneci ?

 

Chimodzi-modzi owelenga zoleyembedwa  kuti anawelenga momwe ndime zotamanda Mtumiki  woyera Muhammad SAW zinasinthidwa ndi Mirza.

Kulakwira kwa JEHAD ndi Mirza Ghulam Ahmad ndi chitsanzo chutuma kuyesa malamuro a Qur’an. Tingagwiritse nchito chilembedwe Chimodzi.

“ Kucoka lero jehadi ya munthu yomwe icitidwa ndi panga, linakwilidwa ndi kulamulidwa kwa Mulungu. Kuyambila lero, aliyense amene anyamula panga kunyamulura kaafir ndi kuziyitana iye kuti ndi GHAZI ali ku lakwira otumidwayo (SAW), amene ananena kwa zaka 1300 zapita kumbuyo  kuti pambuyo pobwela Messiah olenjezedwa onse ma jehads ali ndi ma panga azatha. Telo pakubwela kwanga KULIBE JEHAD ALIYENSE AMENE ALI NDI PANGA. (Collection of Advertisement p.295, vol.3 ).

“ Kochoka pomwe ndinali mwana kufikila lero pomwe ndiri ndi zaka 65, ndakhara ndiri kugwira nchito ya cholembetsa ndi lirime langa pakufuna kusintha m’tima ya ma Muslim’s kuti akhale a chikondi, a chikhulupiliro ndi a chifundo kwa boma la British ndikucotsa ganizo la jehad m’mtima ya Aslims opusa.” (Kitab-ul-Bariya, (Roohani Khazain Vol 13 p.350).

 

“…Mmalo  Boma la  Azungu (British) ndaulitsa ndikufalitsa timapepala 50,000 mdziko lino (India) ndi maiko ena a chi Islam kudzudzula Jehadi…zokoma zake ndi zakuti anthu masauzande ambiri asiya maganizo ao oipa a jihad.” (Roohani Khazain Vol 15 p.114).

 

Mirza ndi Asilamu

Munthu wina anafunsa funso pa za ma Muslims ndipo Mirza anayankha motere ndipo yankhoyi ifunika ku welenga. Zonse ziwiri zinalembedwa mu bukhu lache, Haqeeqat-up-Wahy:

“Funso : Huzoor-e-aali anena mmaro ambiri-mbiri uti sichili chofunika kuyitana KAFIR kuti Kalima-jo (Mnthu amene anayeselela Kalima) ndiponso Ahle-Qibla. Ndi chodziwikilatu  kuti muchitsazo chi, Momineen amene anakhala Kafir pokukana, koposa kumvomelera iye, palibe amene akhala Kafir. Koma mulembe kwa Abdul Hakeem Khan kuti aliyense amene alandila uthenga wanga.

Koma sanandikolole kapena kundivomela ine, iye Muslim. Kuli kutsutsana pa mava awa ndi mau omwe analembedwa kumbuyoku. Poyambilira mu Tiryaqul-Quloob munanena kuti palibe amene akhara Kafir posakukumbukirani koma tsono mulemba kuti pa kukana inu, iye akhala Kafir.

Yankho: Ndi chodabwitsa kuti mpinga munthu amene akana ine ndi munthu amene iatana ine kuti Kafir  ndi anthu osiyana, pomwe mmaso mwa Mulungu ndi munthu m’modzi; chi*****wa amene akana ine  chi*****wa cha kuti azonda ine. Mingu Munthu wabodza-kuchotsako ichi, iye amene sandilora sakhulupirira mwa Mulungu ndiponso mwa Mtumiki. (Haqeeqat-ul-Wahy, Roohani Khazain Vol 22 p.167).

“Kuchotsako ANA ANTHU ACHIWERE-WERE, omwe mitima yao ndi yotsekedwa ndi Mulungu, aliyense akhulupilila mwa ine. (Aina-e-Kamalat-e-Islam, Roohani Khazain Vol 5 p.547).

 

“Mulungu a ndiuza  kuti ali yense emwe walandira uthenga wanga ndipo sanandimvomera, ameneyu sali mu Muslim. (Kalata ya Mirza kwa Dr Abdul Hakeem Khan Patialvi)

 

“Ndiri ndi chifuniro cha Mulungu cakuti iye amene sakulondola ndiponso sazalowa mu B’ith yako ndikukhala otsutsana ndi iwe kapena mdani wako, alibe ulemu kwa Mulungu ndi kwa Mtumiki, Hellish;” (Advertisement mu M’ayaar-ul-Akhyarya Mirza Ghulam p.8)

 

“Lero kumbukirani momwe Mulungu andiuzila kuti ndi chosaroredwa kupemphelera kumbuyo kwa emwe sakhulupilila ndiosafuna, koma kuti Imam yako akhale umodzi wa iwo.” (Arbaeen n° 3, Roohani Khazain vol 17 p.147 just note).

 

MATHERO

Kwa Owelenga!

Ndikhulupilira pa nthawi ino mwaona chomwe munthuyu anali kulingalira. Kudzionetsa kwa kuti anali ndi chikondi cha chikuri cha Utumiki wa UIslam kunali kudziwa lingo lache kuti atsate guru la Ahmadiyyah. Mafunso omwe muyenera kuzifunsa inu nokha ndi aya;

Kodi zilembedwe za m’bukhuri ndizoona ?

Ngati ndizoona, nanga Mirza Ghulam Ahmad, amene anayamba Ahmadiyyah  anamuyamika mwachoonadi Syedna Muhammad kapena anamunyoza?

Kodi munthu woteleyo ndi olongosoka ?

Ngati nitelo, kodi munthu oteleyi tinganene kuti ndi mu Muslim ?

Nanga nchiani chomwe chipangitsa agulu la Ahmadiyya  kubisa izi zokhuzana ndi munthu amene anayamba gururi ?

Kodi Ahmad ndiolondola weni-weni wa Mtumiki  woyela SAW ?

Kodi ameneyu anali munthu otani ?

Angakhale ziganizo zanu zikhale zotani, Mirza Ghulam Ahmad iye izinena motele:

 

Ndiri unyolo mzanga ! Osati munthu, ndili mbali yosaoneka ya munthu ndi malo mvetsa manyazi ku anthu. (Tanthauzo La mau mu Urdu ndi malo yabisika ya anthu olemba)

(Braheen-e-Ahmadiyya V, Roohani Khazain vol 21 p.127 ).

Tipempha Allah aonetsa kuwara kwa Islam ku onse omwe anasochela chi*****wa cha zi chilidwe zotelezi mu dzina la Islam. Allah achinjilize chikhulupililo cha ma Muslims onse ku zoipa zoterezi.

Ameen.

Mtendele ukhale kwa iwo amene olondora njira yoona. 

ANTI AHMADIYYA MOVEMENT IN ISLAM

SYED ABDUL HAFEEZ SHAH

DR SYED RASHID ALI

P.O BOX 11560

Dibba Al Fujairah

United Arab Emirates

Fax (9719) 442846

http://alhafeez.org/rashid/

rasyed@emirates.net.ae

 

الصفحات[ 1] [2]
اضيف بواسطة :   admin       رتبته (   الادارة )
التقييم: 0 /5 ( 0 صوت )

تاريخ الاضافة: 26-11-2009

الزوار: 4948


المقالات المتشابهة
المقال السابقة
Writings Speak
المقالات المتشابهة
المقال التالية
AlFatwa No. 8
جديد قسم مـقـالات الموقـــع
القائمة الرئيسية
البحث
البحث في
القائمة البريدية

اشتراك

الغاء الاشتراك